Ndondomeko za bungwe la ILO zoyenera kutsata pankhani ya HIV/AIDS pa ntchito

The code provides invaluable practical guidance to policy-makers, employers’ and workers’ organizations and other social partners for formulating and implementing appropriate workplace policy, prevention and care programmes, and for establishing strategies to address workers in the informal sector. It is the product of collaboration between the ILO and its tripartite constituents, as well as cooperation with its international partners.

HIV/AIDS ikuwopseza kwambiri kumbali ya kagwiridwe ka ntchito: ikukhudza gulu la anthu limene limagwira ntchito modalilika ndi kubwezera mmbuyo phindu, kupitilira apo, HIV/AIDS ikuchititsa kuti makampani kapena mabizinesi amitundu yonse azitaya ndalama zambiri pa katundu wawo chifukwa chakusagwira bwino ntchito kwa anthu, komanso kutaya ndalama zambiri polipira anthu amene sangathe kugwira ntchito bwino chifukwa chodwala, ndiponso kutaya maluso osiyanasiyana ndi ukatswiri pa ntchito. Kupitilira apo, HIV/AIDS ikusokoneza ufulu wa anthu pa ntchito, makamaka chifukwa chakuti anthu amene ali ndi AIDS ndi amene akukhudzidwa ndi matendawa, anzawo amawasala ndi kuwanyoza. Mliliwu ndi zotsatira zake, zikuzunza kwambiri magulu a anthu monga amayi ndi ana, amene amakumana ndi mavuto ambiri kale chifukwa chakusatetezeka kumene kulipo. Izi zikuchititsa kuti kusiyana kumene kumakhalapo pakati pa amuna ndi akazi (jenda) komanso mchitidwe wogwiritsa ntchito ana mosafanana ndi msinkhu wawo
zikulirekulire. Ichi ndi chifukwa chake bungwe la ILO ladzipereka kunena motsindika podzera m’ndondomeko zoyenera kutsata pa nkhani ya HIV/AIDS ndi pa ntchito. Ndondomekozi zithandiza kwambiri kuchepetsa kufala kwa mliliwu, mavuto amene amabwera chifukwa cha HIV/AIDS kwa anthu ogwira ntchito ndi mabanja awo ndi kupereka chitetezo ndi chithandizo kuti anthu athe kukhala ndi moyo wabwino ngakhale matendawa akadalipo. M’ndondomekozi muli mfundo zikuluzikulu zomwe zingathandize polimbana ndi mliliwu pa ntchito, monga; kuzindikira ndi kuvomereza HIV/AIDS pa ntchito, kusasala anthu amene ali ndi HIV/AIDS pa ntchito, kupereka mwayi ofanana kwa amuna ndi akazi, kuyezetsa magazi ndi kusunga zotsatirazo mwachinsinsi, kupatsa mwayi ogwira ntchito kukambirana za moyo, chitetezo ndi chisamaliro komanso chithandizo.